Tinakumana Ku Mpira

Masewelo a mpira atatha anthu anali pikitipikiti kutuluka paja pa stadium yo.Tsikana uja ndiyemwe anatuluka moyambilira,ine ndi Noel tinatuluka pambuyo pake.M’mene timakafika paja pa stadiumyo tinapeza tsungwana uja akukangana ndi anyamata ena,zimaonesa ngati panali kusavana ndi anyamatawo.

Tsikanayo anawachokera anyamatawo komabe anyamatawo amangomusatila pa mbuyo uku akumulozaloja zala. Ine ndi Noel tinaganiza zolondola tsikanayo pambuyo kuti tione chomwe anyamatawo amafuna kupanga.

Anyamata aja amangomulondola pambuyo kenako taona afika powolokera nsewu.Onse anaima kaye mbali mwa nsewuwo kudikira kuti galimoto ziduse,ine ndi Noel nafe tinafika pompo ndikuima pheee anga sizikutikhuza.

Galimoto zinadusa, mpata owolokera unapezeka apa pomwe anyamatawo pamodzi ndi tsikana uja anawoloka,nafeso tinaoloka nawo limodzi.Apa kuti dima utagwa nyali za nsewu zikuyaka paliponse.

Tizangoyenda pang’ono tsikana uja anakhotela nsewu wafumbi, anyamata ajaso anakhotela nsewu omwewo.

Anangoyenda pangono nyamata modzi anamugwila tsikana uja ndikuyamba kumumenya .Tsikanayo naye anabwezela mbamayo kenako anayamba kulimbanam

Ine ndi Noel tinathamangila pamalopo kukalesesa ndewuyo.Anyamata aja atawona kuti tili mbali ya tsikanayo anathawa.

Titaona kuti anyamatawo athawa tinamutenga tsikanayo kumapelekeza.

Dzina lake anali Charity tsikana woyela ali wochepa thupi,kunena zamaonekedwe anali mwana kuwala weniweni.Titafusa chifukwa chomwe anyamatawo amamunenyela iye anati ,nyamata modziyo anali chibwenzi chake koma chibwenzi chinatha kamba koti tsikanayo amakana kugonana naye nyamatayo nde akufuna amubwezele ndalama zake zomwe anamudyera ali pachibwenzi.

Ine ndi Noel tinayamba kuseka coz zachikale kumenya mkazi ndicholinga choti akubwezele ndalama zomwe anadya muli pachibwenzi.
Tinapelekeza tsikanayo mpaka takasiya kwawo,tinangopasana ma number a phone ndikumabwelera.Tikubwelera tinawaona anyamata aja akubwera mbuyo mwathu koma ulendo uwo anali atatengana gulu 🏃🏃🏃 RUN

To be continued

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *