YONECO iyendera anthu pa msasa wa anthu othawa madzi ku Mangochi

Olemba: Issa Prince Chimwala

Bungwe la Youthnet and Counseling (YONECO) lachiwiri linayendera anthu omwe akukhala pamsasa wa anthu othawa madzi osefukira kwa Chapola mdera la mfumu yaikulu Chimwala ku Mangochi. Pa Ulendowu, a Grant Dulla anapempha anthuwa pa msasawu kuti adzikondana komanso kukhulupirika kwa okondedwa awo.


“Nthawi ngati ino pamafunika kukondana pakati pa wina ndi nzake, mzanu ngati wachoka ndipo mwana wake anatsala ndipo akulira, msamaleni. Kwa anthu apabanja tikupempha kuti pakhale kukhulupirika. Sibwino kupita kunja mkumakapanga zibwezi chifukwa mapeto ake tidzatenganso matenda. Ife ngati bungwe la YONECO tidzibwera pamsasa pano kuonetsetsa kuti mukuthandizidwa moyenera”. Anatsiriza choncho.


Pa ulendowu, a Dulla analinso ndi Issa Chimwala yemwe ndi ophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana kuchokera ku bungwe la NICE. Mkuyankhula kwawo a Issa Chimwala, anapempha adindo oyang’anira ngozi zogwa mwa dzidzidzi mderali kuti awasamalire anthuwa momwe angathere komanso anapempha anthu akufuna kwabwino kuti abwere adzathandize anthuwa pa mavuto omwe akukumana nawo.


M’modzi mwa a komiti ya Ngozi zogwa mwadzidzidzi a Rajab Hassan anathokoza mabungwe a YONECO ndi NICE kamba kodzacheza ndi anthuwa, iwo anati izi ziwalimbitsa mtima. Anthuwa anathokozanso a Komiti pamsasawu kamba ka chikondi ndi chisamaliro chomwe akuwapatsa.
Pamsasawu pali mabanja 70 omwe nyumba zawo zinagwa kamba ka mvula yamphamvu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Please disable your adblocker or whitelist this site!