Apolisi Adatiuza Kuti Akhala Busy Mpaka December,

Akuluakulu a gulu lomwe likudzitcha kuti Mzika Zokhudzidwa ati apolisi adawauza kuti sakhala ndi mpata kufikila mwezi wa December ndipo kuti dongosolo lawo za zionetsero silingatheke pakadalipano.

Iwo anena izi Lachitatu pa msonkhano wa olemba nkhani munzinda wa Lilongwe pomwe ati ngati angalandire chilolezo ku bwalo la milandu apitilira ndi zionetsero zawo mawa, Lachinayi.

Gululi likufuna kuti apolisi amange apolisi anzawo omwe akuti akudziwa kanthu pa zomwe zidachitika pa imfa ya Emmillie Halimana Noel pa 17 October chaka chino.

M’modzi mwa akuluakulu a gululi, Wells Khama wati akukhulupilira kuti akuluakulu a polisi adalandira ndalama zokwana 20 million kwacha kuti abise za imfayi.

Apolisi sadapezeke msanga kuti ayankhepo pa izi koma masiku angapo apitawo m’neneri wawo, Peter Kalaya adati akufufuzabe za nkhaniyi ndipo sizowona kuti akubisa wa polisi aliyense.

DC wa boma la Lilongwe, Dr. Lawford Palani anati aimitsa kaye zionetserozi ati kamba koti Lachinayi apolisi akhala otanganidwa ndi ntchito zina; zomwe gululi lati nzosamveka ndi pang’ono pomwe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *