Titathana ndi madando a Flames, yafikanso nthawi yoyedzekana mu mpikisano wa Airtel Top 8 omwe uyamba masana a tsiku la lero pa bwalo la Kamuzu nzinda wa Blantyre pakati pa FCB Nyasa Big Bullets komanso Civil Service United.
Matimu awiriwa anakumananso posachedwapa mu mpikisano wa FDH, pamene anyamata a Civo anaona ngati akulota nthawi yotha itha Precious Phiri, atawatulutsitsa misonzi yonyung’unya pogoletsa chigoli chimodzi chokhacho.
Wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu Wa FCB Nyasa Big Bullets, Mike Ngore, wati akonzeka kuchita bwino pozindikira komwe akuchoka pamene anagonja ndi Blue Eagles mu mpikisano wa FDH Bank masabata awiri apitawo.
Iye wati akungoyenera kupambana kuti apereke chiyembekezo kwa otsatira timuyi.
”Munthu amaweruzidwa m’mene wadzukira akagwa osati mmene wagwera, ” watero Ngore.
Koma mwina Civo chiyembekezo ndi kukhala nacho chochita bwino pa bwalo la Kamuzu pamene mu mpikisano ngati omwewu inapambanako 2-1 koma Bullets inapitilira chifukwa masewero oyamba omwe analipo pa bwalo la Civo, Bullets inapambana 2-0.
Pakadali pano, Bullets ndiyomwe ikusunga chikhochi pomwe inagonjetsa timu ya Mafco 3-0.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!