Mphuzitsi wa timu ya mpira wamiyendo yadziko lino Patrick Mabedi wati tsopano agwilitsa ntchito masewela omwe atsala odzigulira malo mumpikisano wa Afcon ngati mbali yokozekela masewera odzigulira malo mumpikisano wapadziko lonse a World Cup.
A Mabedi ayankhula izi kutsatira pomwe timuyi yalephera kudzigulira malo mu mipikisano wa AFCON kutsatila kugonja ndi team ya Senegal 1-0 pamasewero omwe anachitika lero pabwalo la zamasewero la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.
Malingana ndi a Mabedi ati timu yadziko linoyi siikuchita bwino kaamba kosakozekera bwino kotero masewero omwe atsalawa apeleka danga lokoza pomwe pakumavunda khola cholinga choti timuyi iyambe kuchita bwino.
Pakadali pano Flames ili pansi penipeni pa gulu L ndipo ilibe ngakhale point ndiimodzi yomwe kuchoka mumasewero anayi omwe yasewera.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!