By Issa Chimwala — Machinga
Chisankho cha chipululo cha UDF ku Machinga North East chasokonekera, ngakhale bwalo lalikulu ku Zomba lidalamula kuti chichitike pa 22 July.
Izi zatsatira pomwe Denis Maloya, mmodzi mwa omwe akufuna kupikisana, kudzera mwa loya wake Masurool Daud, anakapempha bwalo kuti chipanichi chichititse chisankho cha poyera pambuyo poti chinatsutsa kuti ena apikisanepo.
Ngakhale chipanichi chinapereka tsiku lachisankho, zomwe zinakakamiza anthu ambiri kufika pa bwalo lamasewero la Chaka ku Malundani, chodabwitsa nchakuti Denis Maloya yekha ndiye anafika. Ena omwe akufuna kupikisana nawo, kuphatikiza Nix Kamphulusa komanso ochititsa chisankho, sanawonekere.
Mphekesera zikusonyeza kuti akuluakulu a chipanichi anali ku Mtaja, komabe sichikudziwika bwinobwino chifukwa chake chisankhochi chinachedwa.
Mmodzi mwa anthu amene anafika pamalopo, Shaibu Rajab, adati:
“Chipanichi chingotiuza momveka bwino ngati chisankho chichitike kapena ayi. Tikufuna tidziwe ngati akufuna kuphwanya chigamulo cha khoti mwadala. Tafika pano 7 koloko, koma mpaka 2 koloko palibe zomwe zikuchitika.”
Pakadali pano, anthu akuyembekezera mawu a UDF pa zomwe zichitike mtsogolo.