Mlangizi wa boma pa nkhani za malamulo Thabo Chakaka Nyirenda wasemphana zochita ndi komiti ya Public Appointments-PAC pa nkhani yoti yemwe adali wachiwiri kwa mkulu wa NOCMA, mai Hellen Buluma akaonekere ku nyumbayi kuti akafotokoze mwatchutchutchu zomwe adalemba mu kalata yawo yosiya ntchito.
Mwa zina, a Buluma adati wapampando wa board ya NOCMA yemwenso ndi mlembi mu ofesi ya mtsogoleri wa dziko ndi nduna zake, mai Colleen Zamba, akuluakulu ena a chipani cha MCP komanso a boma ankawakakamiza kuti adzipereka ma contract mwachinyengo.
Koma a Chakaka Nyirenda auza Sipikala wa nyumba ya malamulo, Catherine Gotani Hara kuti a Buluma komanso a Zamba asawonekere ku komiti-yi pomwe PAC yati ipitilira ndi ganizo lake lofunsa awiriwa.
Kodi nkoyeneradi kuti mai Buluma ndi mai Zamba ayankhe mafunso?