Olemba Yassin Achucha Mailosi
M’modzi mwa omwe adzapikisane nawo pa mpando wa Phungu wakunyumba ya Malamulo kudera la Mangochi Nkungulu a Hameed Kasoz Kasondo apempha anthu akuderali kuti akalembetse mkaundula wa chisankho mwaunyinji kuti adzathe kusankha atsogoleri akumtima kwawo pa chisankho cha chaka chamawa. A Kasoz amayankhula izi pa ulendo wawo oyimayima (whistle stop tour) omwe anali nawo pa 2 December 2024. Iwo anapempha anthuwa kuti akadzalembetsa mkaundulayu adzasankhenso atsogoleri amasomphenya osati momvera munthu chisoni.
“Atsogoleri omwe tinawasankha mu 2019 sanatithandize, akanika kutukula dera lino ndipo palibenso chifukwa chowasankhiranso. Anthu aku Nkungulu ndi olimbikira pa ntchito zosiyanasiyana ndipo pamafunika kuti atsogoleri omwe timawankha aja adzithandizira kuti miyoyo ya anthu akudera lawo itukuke. Taganizani msewu ochokera pa Mpale kupita ku Chisawa ndi oyipitsitsa chonsecho tiri ndi thumba la ndalama zachitukuko koma limagwiritsidwa ntchito ngati ndalama Za munthu. Ulendo uno musankhe mtsogoleri yemwe adzaike zofuna zanu patsogolo, mtsogoleri yemwe azidzakumana nanu mosavuta, azidzapezeka kumikumano yamakomiti achitukuko monga ADC ndi VDC kuti akamve madandaulo achitukuko ochokera kwa anthu ake osati mtsogoleri omapezeka kudera chisankho chikayandikira, ichi nchifukwa chake ndikufuna kudzapikisana nawo pa chisankho cha chaka chamawa kuti ndibweretse utsogoleri okomera anthu onse. Ndikukulonjezani kuti zitukuko zidzafika ponseponse posatengera komwe ndinavoteredwa kapena ayi ndipo aliyense adzathandizidwa posatengera chipani kapena mtundu. Mafumu naonso ndikufuna azidzapatsidwa ulemu, osati mtsogoleri onyoza mafumu ayi”, anatsiriza choncho a Kasoz. Kasoz ndi m’modzi mwa anthu omwe aonetsa chidwi chodzapikisana pamasankho achipulula kuchipani cha DPP ndipo Iwo adaperekezedwa pamdipitiwu ndi khansala wa DPP wa Nkungulu Ward a Martin Milanzi, Constituency Governor a Dunkan Kili ndi Committee yawo yonse ya Constituency komanso District Governor wa DPP m’bomali a Kadango.
Ulendo wamdipitu unayambira pa Chipalamawamba Primary School ndipo unakathera pa Chisawa Primary School.