Azimayi akwiya ndi ganizo la kudula azimuna pa milandu yogwiririra

images 1 2

By Suleman Chitera

Azimayi ambiri m’dziko muno akusonyeza kukwiya kwakukulu ndi ganizo lomwe likukambidwa m’Nyumba ya Malamulo loti azimuna opezeka olakwa pa milandu yogwiririra azidulidwa.

Malinga ndi azimayiwa, chilango chimenechi chingayike miyoyo ya azibambo ambiri pa chiopsezo, chifukwa akuti chikhoza kugwiritsidwa ntchito molakwika, makamaka pa milandu imene ikhoza kukhala yonamiziridwa.

Iwo akunenanso kuti khalidwe la ana atsikana ena masiku ano likuthandiza kukulitsa milandu yogwiririra, ponena kuti ena mwa atsikanawo amakhala ndi makhalidwe okopa azibambo, zomwe zingapangitse kuti zinthu zisamayende bwino. Choncho, akufuna kuti boma ndi mabungwe osiyanasiyana ayike patsogolo kulimbikitsa maphunziro a khalidwe, upangiri, komanso zipembedzo kuti zithandize kukonza makhalidwe a achinyamata.

Azimayiwa awonjezera kuti mabanja ambiri akusokonekera chifukwa cha kusowa kwa upangiri ndi ulemu pakati pa achinyamata, ndipo izi zikufunika kuthandizidwa mwachangu osati kungoyang’ana pa chilango chokha.

Ponena za chilango chomwe chikukambidwachi, iwo akuti chikhale chofanana kwa aliyense popanda tsankho. Ena mwa iwo akupempha kuti ngati chilango chikhazikitsidwa, chigwire ntchito mofanana kwa onse—kapena kumangidwa kwa olakwa onse—osati kungolunjika pa amuna okha.

Azimayiwo aopsezanso kuti atha kupanga zionetsero ngati Nyumba ya Malamulo itapitiriza ndi ganizo limene iwo akuti silikuwonetsa chilungamo komanso lingayambitse mavuto ambiri m’dziko muno.

Nkhaniyi ikubwera pamene akuluakulu a boma akupitiriza kukambirana njira zosiyanasiyana zolimbana ndi milandu yogwiririra, yomwe yakhala ikukwera m’dziko muno, pomwe ena akutsindika kufunika kokhazikitsa malamulo okhwima pomwe ena akufuna njira zokhazikika zomwe zingathetse vutoli kuyambira pa mizu yake.

See also  Fuel Crisis Strikes Lilongwe Again as Long Queues Resurface

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *