Akuluakulu ku nthambi yoona za chilengedwe ati nzosatheka kuti dziko la Malawi liloleze anthu kuyamba kuweta Ngaka (Pangolin).
Brighton Kumchedwa, nkulu woona za malo osungirako nyama ndi zachilengedwe zina wanena izi lero kunyumba ya malamulo, pomwe amayankha funso lochoka kwa phungu wa dera la Chiradzulu East Joseph Nomale yemwe anadabwa kuti nchifukwa chani boma likumanga anthu omwe akupezeka ndi Ngaka mmalo mosiya kuti anthu adziweta ndikumagulitsa.
Nomale adati Ngaka ikufunidwa ndi maiko ambiri ndipo ogula akumagula nyamayi ndi ndalama yakunja ya Dollar, zomwe zingapindulire dziko la Malawi ngati ataloleza kuti anthu adziweta mmakomo mwawo.
Malingana ndi Nomale, nzodabwitsanso kuti aboma akuti Ngaka ndi nyama yotetezedwa chonsecho nyamayi ikumapezeka ikungoyenda mminda mwa anthu.
Koma Kumchedwa wati zomwe a Nomale akunena nzosatheka chifukwa Ngaka ndi nyama yotetezedwa pa malamulo a dziko lino Komanso malamulo ena a dziko lonse lapansi omwe anaika nyamayi pa ndandanda wa nyama zomwe moyo wake uli pa chiopsezo.
Kumchedwa watinso nzosatheka kuweta Ngaka pakhomo chifukwa choti si nyama yoti munthu utha kumadyetsera.
“Ena akaba Pangolin amapezeka akuikakamiza nyamayi kuti idye nsima, izi zamapeleka chiopsezo ku moyo wake ndipo itha kufa. Izi zikusonyeza kuti Pangolin si nyama yoti utha kuweta pakhomo chifukwa imazisakira yokha zakudya ngati nyerere zomwenso zimapezeka kwambiri nkhalango ndi malo ena”, adatero Kumchedwa.
Pakadali pano Werani Chilenga wapampando wa komiti yoona zachilengedwe wauza anthu kuti atalikirane ndi nyamayi ponena kuti aliyense opezeka nayo akalowa kundende.