Musapite Ku China: tizivutika tonse — Suleman

Phungu wadera la Blantyre City South east Sammeer Suleman ati mtsogoleli wa dziko lino asapite ku China pa ulendo omwe wakonzedwa masiku akubwerawa.

A Chakwera akuyembekezeka kupita m’dziko la China komanso Ku United States of America kuchoka pa 6 mpaka pa 9 September.

Suleman ati mtsogoleli-yu akhale mdziko mommuno ndipo akhale ndi a Malawi pa nthawi yakukwera kwa mafutawa komanso zinthu zina.

Koma poyankhapo, mtsogoleli wa nyumbayi a Richard Chimwendo Banda ati nkofunika kuti mtsogoleli wa dziko lino apite ku China pofuna kuti ubale wa dziko lino ndi China upite patsogolo.

Iwo ati: “anthu akuvutika kale mdziko muno ndipo mkosafunika kuti mafuta a galimoto akwere.Boma lipeze njira zina zokonzera zinthu pa nkhaniyi.”

Suleman wapempha mkulu wabungwe la Consumers Association of Malawi(Cama) John Kapito kuti atule pansi udindo wake.

A Suleman omwe amayankhula kunyumba ya malamulo lachiwiri masana ati a Kapito alephera kutumikira a Malawi ngati mkulu wabungwe la Cama.

Izi zikudza pomwe a Kapito awuza nyumba zowulutsa mawu zina m’dziko muno kuti ndikoyenera kuti bungwe la Mera likweze mafuta a galimoto padakali pano pofuna kuti mafuta adzipezeka mosavuta.

Pomaliza kulankhula kwao a Sameer Suleman apempha mkulu wa bungwe la Consumers Association of Malawi, CAMA a John Kapito kuti atule pansi udindo wawo

A Suleman ati: “A Kapito akhalitsa pa udindowu.Kapito ndi mmodzi mwa anthu omwe anayambitsa nkhani yoti mafuta a galimoto akwere mdziko muno.”

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *