Yelekezani Dala Kukweza Mafuta Timatcha”_ DPP

Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chati chikutsutsabe ganizo lakuti boma likweze mafuta agalimoto mdziko muno.

Mtsogoleri wambali yotsutsa boma kunyumba mnyumbayi George Chaponda wanena izi pamsonkhano wa atolankhani omwe mbali yotsutsa boma pamodzi ndi ayimila zipani za UTM komanso AFFORD zinachititsa lero kunyumba yamalamuloyi.

Malingana ndi a Chaponda aMalawi ambiri akuvutika kotelo kukweza mafuta pakali pano kuthu kupsinja aMalawi ambiri maka a mmadera akumudzi.

Mwazina a Chaponda anati boma likuyenela kutsatila njira zina zomwe zingathandize kukoza chuma cha dziko lino monga kuchepetsa ma ulendo amtsogoleri wadziko lino.

“Posachedwapa boma lalandila mafuta agalimoto malita oposa 30 miliyoni kuchokera kudziko la DRC posinthana ndi asilikali athu ankhondo omwe aka omwe akadatgandiza kuti mitengo isakwere koma mafutawo wina wagwilitsa ntchito, ndiye lero aziti akweze mafuta?

“Ndipotu tikuti angoyelekeza kukweza mafutawo, tsiku lomwe akwezelo ifeyo tituluka ndipo kununkha mphira.”_ watelo mmodzi mwa aphungu a DPP a Sameer Suleman.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *