![](https://malawifreedomnetwork.com/wp-content/uploads/2025/02/FB_IMG_1738775221319-1024x868.jpg)
Kukana kukweza mtengo wa mafuta a galimoto kwazetsa ndemanga zosiyanasiyana pakati pa akatswiri omwe amalankhulapo nkhani zosiyanasiyana m’dziko muno.
Ena akuti izi ndi ndale chabe kamba koti mtsogoleri wa dziko linoyu akuyang’ana za chisankho chomwe chiliko m’mezi wa September chaka chino, pomwe ena ayamikira ganizo la mtsogoleriyu lokana kukweza mtengo wa mafuta a galimoto ndi K30 pa K100 iliyonse.
Izi zikudza pomwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akana kukweza mtengowu ndi K30 pa K100 iliyonse malingana ndi mabungwe komanso anthu omwe amachita malonda a mafutawa amafuna.
Malinga ndi Andrew Kaponya, boma likupanga ziganizo poyang’ana zisankho zomwe zikubwerazi kamba koti akuopa kuti mafuta akakwera mtengo, katundu osiyanasiyana akwera zomwe zipangitse kuti anthu adere nawo nkhawa.
“Anthu akaona kuti zinthu zakwera, ada kukhosi ndi mtsogoleri wa dziko lino zomwe zikuwaopsa pamene dziko lino likupita ku chisankho posachedwapa,” watero Kaponya.
Katswiri pa nkhani za chuma Milward Tobias wayamikira mtsogoleriyu pokana kukweza mtengo wa mafuta ponena kuti kukweza mu makwacha sikungabweretse ndalama yakunja ya mtundu wa Dollar yomwe timagulira mafutawa.
Tobias wati vuto lakusowa kwa mafuta m’dziko muno ndi kamba ka kusowa kwa ndalama ya kunja ya Dollar yomwe timagulira kotero kukweza mtengo pakadali pano ndi kungophinja aMalawi chabe.
Komabe iye waonjezera kunena kuti vuto la kusowa kwa mafuta lili pakadali pano ndi vuto la utsogoleri wawo omwe ukulephera kubweretsa mayankho okhazikika pa vutoli.