Victoria Kingstone sapikisana nawo pa chisankho cha chipulula ku Mangochi

Phungu wa dera la pakati pa boma la Mangochi wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) Victoria Kingstone wati sapikana nawo pa chisankho cha chipulula chomwe chipanichi chikuyembezereka kuchititsa mawa pa 3 May.

A Kingstone ati mwa ichi azapikisana nawo ngati phungu wa nyumba ya malamulo pa chisankho chapa 16 September ngati phungu oima payenkha koma izi sizikutanthauza kuti atuluka chipani cha DPP.

Izi zikudza pamene pali mphekesera kuti kuderali, chiwerengero cha nthumwi zomwe zikuyenera kusankha yemwe adzaimire chipanichi ngati phungu chaonjezeleka kusiyana ndi chikonzero cha komiti ya chipanichi m’derali.

“Adindo atitsekera chitseko, olo kuti tipange nawo chisankho ndaona kuti sichikhala cha bata ndi mtendere nde ine ndachiona cha nzeru kusapanga nawo komabe ndine membala wa DPP”. Atero a Kingstone.

Kudera lomweli, anthu enanso asanu ndi mmodzi 6 a chipani cha DPP omwe amafuna kudzayimira nawo pa udindo wa khansala ati sapikisana nawo pa chisankho cha chipululachi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *