DZAKA 12 CHIFUKWA CHOPEZEKA NDI NDALAMA ZA FAKE

Bwalo la Magistrate ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota lalamura kuti a Yesaya Quoto a dzaka zakubadwa 24, akakhale ku ndende ndi kugwira ntchito ya kalavula kwa dzaka 12, kamba kopezeka ndi ndalama zama k5000 a pepala za chinyengo zokwana k575, 000.

Quoto anamangidwa pa 28 March, 2022 pa Dwangwa Trading Center atapezeka ndi ndalamazi pomwe ankafuna kutumiza pa airtel Money kwa mayi wina pamalopo.

Agent wa airtel money-yu atazidabwa ndalamazo zomwe zimakwana k60, 000, adayitana anzake, ndipo adaganiza zodziwitsa apolisi apa Nkhunga police station omwe anabwera nkuzamanga oganiziridwayu.

Apolisi atamusecha anamupezanso ndi ndalama zina za chinyengo zokwana k115, 000 zokhala ndi serial number ya AA7915614.

Apolisi anapitanso kunyumba kwake kukalanda machine omwe akukhulupilira kuti ankagwiritsa ntchito popanga ndalamazi.

Apolisi anamutsegulira Quoto milandu itatu; opezeka ndi ndalama za chinyengo popanda chilolezo, opezeka ndi machine opangira ndalama za chinyengo, komanso opanga ndalama za chinyengo.

Bwalo la milandu linapeleka dzaka 4 ku mlandu oyamba, dzaka zina 4 ku mlandu wachiwiri, komanso dzaka 12 ku mlandu wachitatu. Zilango zonsezi zigwira ntchito nthawi imodzi.

Yesaya Quoto amachokera m’mudzi mwa Mwerekete, T/A Mthwalo, m’boma la Mzimba.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *