Takonzeka kugonjetsa Wanderers – Kamanga

Mphunzitsi wamkulu wa timu ya Kamuzu Barracks (KB), Charles Kamanga, wati anyamata ake akonzeka kuvinitsa chindendelinde timu ya Mighty Mukuru Wanderers mawa lino, lachinayi, pa bwalo la Civo mu nzinda wa Lilongwe.

Kamanga wati akuzindikira kufunika kopambana masewerowa ngakhale sizikhala zophweka kutero.

Iye wati ngakhale asowe zintchito za Olson Kanjira, yemwe ndi ovulala, ndi nthawi ya osewera ena kuti aonetsa kuti atha kusewera.

Pakadali pano mphunzitsi wamkulu ongogwirizira ku timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati akonzeka kupeza chipambano pamasewero amenewa.

Mwase wati ngakhale padutsa masewero asanu osapezako chipambano pamwamba pa KB, koma chiyembekezo alinacho kuti chipambano chipezeka.

Manoma ali panambala yachiwiri ndi mapointi 35 pa masewero 18 omwe asewera pamene KB ili panambala 5 ndi mapointi 28 pa masewero 18 omwe asewera.

Komatu zidebe ndimalingaka akamazalira pa bwalo la Civo kudzakhala ku Karonga kwayakaso moto, pamene Chitipa United idzakhala ikusewera ndi Silver Strikers.

Timu ya Silver Strikers chiyambileni ligi ya Tnm chaka chino sinalaweko ululu wa kugonja, komabe tidikire mawa poti paja amati kwaeni kulibe mkuwo.

Chitipa United ili pa nambala 13 ndimapoint 16 itasewera masewero 18, pamene timu ya Silver Strikers ili pamwamba ndimapointi 43 pamasewero 17 omwe asewera.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *