Nkhalakale pa ntchito ya utolankhani yemwenso ndi m’modzi mwa akuluakulu pa wailesi ya kanema ya Mibawa a Wellington Kuntaja ati ayamba ndale ndi cholinga chofuna kuthandizira kusintha zinthu m’dziko muno.
Malinga ndi Kuntaja, kuyamba ndale sikukutanthauza kuti asiya kugwira ntchito zomwe komanso kupanga mapologalamu pa kanema ya Mibawa koma kutsegula makomo ena a moyo wawo komanso kampani ya Mibawa.
“Ngati atolankhani, timakhala tikuzuzula m’chitidwe wina omwe a ndale amakhala akuchita koma tsopano yakwana nthawi kuti tichitepo kanthu,” watero Kuntaja.
Kuwonjezera apo, iwo ati akhala akufuna kuchita ndale moyo wawo wonse kotero nthawi yakwana kuti achitepo kanthu.
Mkulu oyang’anira kampani ya Mibawa a John Nthakomwa ayamikira a Kuntaja pokwaniritsa masomphenya awo ndipo awafunira mafuno abwino. M’mau awo, a Nthakomwa ati “Mibawa siipanga za ndale, ndipo a Kuntaja saloledwa kutenga mbali pa mapologalamu ena aliwonse okhudza ndale za m’dziko muno pa kanema wa Mibawa’.
Kuwonjezera apo iwo ati a Kuntaja azitenga mbali pa mapologalamu omwe azithandiza achinyamata potengera ukadaulo wambiri umene alinawo.
A Wellington Kuntaja anakapikisana nawo pa mpando wa m’neneri wa chipani cha People’s – PP ku msonkhano wake waukulu omwe unachitikira mu mzinda wa Lilongwe.
Iwo anagonja ndikukhala wachiwiri kwa m’meneri wachipanichi a Ackson Kalaile Banda.
Wolemba Deborah Kulinji Jenala