Mtsogoleri wa chipani cha MCP Dr. Lazarus Chakwera wadzudzula omwe akumalowetsa imfa ya wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino wakale Dr. Saulos Chilima munkhani za ndale.
Iwo ati anthu atenge zomwe zidatuluka mulipoti la akatswiri am’dziko la Germany komanso madotolo a m’dziko muno zokhudza ngozi ya ndege yomwe idapha a Chilima ndi anthu ena 8.
Mtsogoleriyu wati iwo ndi a Chilima anagwilizana zopanga ndale zotukula miyoyo ya a Malawi osati ndale zopakana matope.
Iwo ati ndi mtsogoleri yemwe wachita zitukuko zosiyanasiyana m’dziko muno ndipo athokoza anthu achipanichi powapasanso mwayi oti apitilize kutsogolera chipanichi.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!