Wolemba: Burnett Munthali
Mkulu wa Premier Bet m’chigawo cha pakati, a Moses Namacha, wati masewero a Premier Lotto omwe adayima mu 2023 abwereranso mwamphamvu.
Iwo ati a Malawi ayembekezere zosangalatsa zambiri chifukwa masewerowa akubwera ndi zatsopano komanso mwayi kwa aliyense.
A Namacha ananena izi ku mzinda wa Lilongwe pamene Premier Bet inkakhazikitsanso masewero a Premier Lotto m’chigawo cha pakati.
Iwo anati cholinga cha kubwezeretsa masewerowa ndi kupatsa mwayi anthu osiyanasiyana omwe nthawi zina samatha kulowa muma shop a Premier Bet.
Iwo anafotokoza kuti Premier Bet ili ndi chidwi chowonjezera mitundu ya masewero kuti makasitomala azitha kusankha zomwe zimawapatsa chisangalalo.
Read also: Holy Guardian Angels Conducts Fundraising as Part of Strategy for Self-Reliance
Read also: Khombe’s abduction: Fact or fiction?
Read also: Mozambique President visits Malawi Parliament and Kamuzu Mausoleum
Komabe, a Namacha anachenjeza anthu kuti asamasewere masewerowa pogwiritsa ntchito ndalama zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku.
Iwo anati, “Munthu walandira malipiro apamwezi, usagwiritse ntchito ndalama zake zonse ku masewerowa.”
Anapitiliza kuti, “Timanena mobwerezabwereza kwa makasitomala athu kuti adzipanga masewerawa mosamala chifukwa awa ndi masewera chabe, osati ntchito.”
A Namacha anatsindika kuti masewerowa amayenera kuchitidwa ngati njira yosangalalira, osati njira yoti munthu adalire moyo wake wonse.
Iwo ananena kuti Maere a masewerowa adzachitika kasanu ndi kamodzi patsiku, kupatsa anthu mwayi wopitilira umodzi kuti athe kutenga nawo mbali.
Premier Bet yalonjeza kuti ipitiliza kusintha njira zosewerera kuti zipereke chithumwa komanso chitetezo kwa makasitomala ake.
Read also: Malema: By mourning and praising the queen, you are celebrating colonialism
Read also: THE TRUTH ABOUT THE MK378.4MILLION LOAN BY MR MKANDAWIRE AND MR BATATAWALA‼️
Read also: Kalindo Given President Chakwera Seven-Days To Fire Martha Chizuma Over leaked Audio





