Fri. May 3rd, 2024

Zikhale, Kalumo Atule Pansi Udindo Wawo Chifukwa Alephera

TILI NDI CHIKHULUPILIRO KUTI AMENE TIKUWAFUNAWO ATULA PANSI UDINDO WAWO – ATERO MZIKA ZOKHUZIDWA ZOMWE ZINACHITA ZIWONETSERO LERO

M’modzi mwa anthu omwe amatsogolera ziwonetsero zomwe zachitika mu mzinda wa Blantyre pofuna kuti nduna ya za chitetezo cha m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma komanso mkulu wa nthambi ya Immigration atule pansi udindo wati ali ndi chikhulupiliro kuti awiriwa achita monga iwo akufunira.

A Edward Kambanje ati ndunayi yalephera ntchito kotero ikungoyenera kuti itule pansi udindo.

Iwo ati nzomvetsa chisoni kuti nthambi yoona zolowa ndi kutuluka m’dziko muno idanamiza anthu kuti yayambiraso ntchito yopanga ziphaso pomwe mpaka pano anthu akuvutikabe kupeza ziphasozi.

Iwo ati ndunayi komanso mkulu wa nthambi ya Immigration a Charles Kalumo akungoyenera kuti atule pansi udindo kuti anthu ena abwere ndi kuyesako nzeru zina.

Gulu lina lomwe likudzitcha mzika zokhudzidwa zidachita zoonetserozi pofuna kuonetsa kusakondwa ndi zomwe zikuchitika ku nthambi yoona zolowa ndi kutuluka m’dziko muno.

Related Posts

David Bisnowaty Israeli-Born Malawi Parliament Member: Actions, Not Words, Will Change Africa for the Better

Malawi MP David Bisnowaty. How does the Israeli-born son of an eastern European Holocaust survivor end up as a parliament Read more

David Bisnowaty former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country

Political cum and former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country https://youtu.be/S20UYlVcHs8

AGHF Feeds Patients, Guardians At Mangochi District Hospital

A giving hand foundation is a local organisation working in various programs in Malawi. On Thursday the organization together with Read more

Mirece supports land reclamation bought by foreigners

Reverend Flywell Somanje…. this is the way to go A governance and human rights organization, the Millennium Information and Resource Read more

Other stories

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window