Izi zadza chifukwa bread wakwela mtengo kufika pa 1 000 Kwacha m’modzi , m’magolosale ena.
Akuluakulu ena omwe ali ndi ma bakery, akuti mtengo wa tiligu, wakwela padziko lonse, zomwe zachititsanso kukwela kwa mtengo wa ufa opangila bread.
“Chomcho , ufa wopangila bread wachoka pa 36, 000 Kwacha kufika pa 48, 000 Kwacha , thumba limodzi la 50 kilograms,” watelo m’modzi mwa iwo.
Ndipo m’kulu wa bungwe la ogula malonda la Consumers Association of Malawi – CAMA, a John Kapito, wati boma lichitepo kanthu pa nkhani ya mitengoyi, chifukwa anthu m’dziko lino, avutika.
“`