Wolemba: Grecium Gama.
Kusowekera kwa maphunziro kwa aphunzitsi amkomba phala m’boma la Chikwawa kukulowesa maphunzirowa pansi.
Izi zadziwika pamene bungwe la Community forum Organisation Limagawa mabuku komanso zoseweretsa ana ankomba phala m’sukulu za Chisomo Namabvu ndi Mulambe Community-Based Childcare Centre zomwe zikupezeka m’dera la mfumu yaikulu Mulilima komanso Katunga
Poyakhulapo mlangizi wochokera ku offisi yoona chisamaliro cha anthu bomalo , Lysan Mangasanja anati m’sukulu zambiri zikusowekera nthandizo la ndalama zogulira zithu monga mabuku komanso zithu zina zofunikira m’sukuluzo.
Iye anati aphunzitsi ambiri m’bomalo alibe lutso kapena upangiri wophunzitsira ana .
“Tipephe mabungwe komanso anthu akufuna kwabwino kuti abwere azaphunzitse aphuzitsiwa m’cholinga choti ntchito yophunzitsa anawa iyambe kuyenda bwino.
Ndipo mmodzi mwa aphunzitsi apa sukulu ya Chisomo Nambavu adapepha boma kuti liyambe kupereka ndalama kwa aphunzitsi amkomba phala zomwe bomalo lidalonjeza zaka zinayi zapitazo kaamba koti zimabwerezeresa kagwiridwe ntchito kwa alezi ambiri.
” alezi ambiri samakhalandi chidwi chophunzitsa kaamba koti sitimalandirako kathu ndiye tikupepha ganizo laboma lomwe adalonjenza zoyamba kutipasa kangachepe kuti lipitilire mcholinga choti tizitha kugula zosowekera pa moyo wathu”, iwo adagotokoza.
Mkulu wa bungweli Joshua Malunga anati iwo akhala akupephedwa kuchokera kwa alezi komanso akuluakulu amsukulizi kuti awathandize ndi mabuku.
Iwo adati kudzera ma madandaulowa adachiona cha mzeru mkuthandizapo ndi mabuku m’sukuluzo.