Kusamvana kwabuka pomwe ochemelera timu ya Mighty Mukuru Wanderers sakukhutira ndi ziganizo zomwe oimbira masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos Salima Sugar FC, Alfred Chilinda amachita m’chigawo choyamba cha masewerowa.
Zinatengera a chitetezo omwe analowa m’bwalo la maseweroli kukateteza oimbirawa ku ochemerea okwiya omwe amafuna kuti afotokozeredwe bwino za ziganizo zawozi.
Pakalipano osewera a mbali ziwirizi akupumulira pomwe Dedza Dynamos ikutsogola ndi zigoli ziwiri kwa duu mu ligi ya TNM.
Wolemba: Horace Tebulo – DEDZA