Kunena moona khalidwe lotutana mudzi onse kunka nawo ku America sikuti tiwanamize a Malawi wayamba ndi boma la a Chakwera ai; koma ili ndi khalidwe lonyasa lomwe lakhala likusakaza ndalama za dziko lino ndima President onse omwe akhala akulamulira dziko lino oChakwera asanayambe kulamula dziko lino.
Funso n’kumati kodi chavuta ndichani ndi ulendo wa oChakwera?
Vuto la ulendo wa oChakwera likudza kamba koti pakali pano m’dziko muno mulibe ndalama zakunja zomwe zimathandiza kuti tizitha kugula katundu wakunja ofunikira yemwe sitimatha kupanga m’dziko mwathu muno monga: mafuta agalimoto, mankhwala akuchipatala, chakudya, zovala ndizinthu zina zonse zomwe sizipangidwa ku Malawi kuno.
Funso lina nali: kodi panalibe njira ina kupatula yoti oChakwera ndi owatsatira awo akwere ndege apite akayankhule?
Njira inalipo ndipo yakhala ikugwilitsidwa ntchito chilowereni m’boma oChakwera. Iwo akhala akugwiritsa ntchito Skype ndi njira zina poyankhula pa makina a internet omwe amatenga zomwe akuyankhula ali kuno kumudzi kupita ku America.
Kodi zikanathandiza chani pachuma chathu?
Izi zikanasimikizira mayiko onse kuti dziko lathu likusaukira ndalama yakunja ndipo tikufunika chithandizo chamayiko ena.
Ena onse omwe akukumana nawo amene akuti ndi ma investor zinalinso zotheka kuyankhula nawo panjira iyi.
Izi zikanathandiza kuti ma million a ndalama za America omwe awonongedwa pa ulendowu agwire ntchito zothandiza kupeza katundu yemwe tikuvutika poyitanitsa kunja kamba kakusowa kandalama yakunja pakali pano.
Pomaliza, tiwapemphe a president monga m’busa kuti akumbuke mawu a mfumu Solomoni okuti “chilichonse chili ndi nthawi; pali nthawi yolira komanso yosangalara”.