Zifukwa Zomwe Tikufunira Bright Msaka Adzatitsogolere

KUTHETSA KATANGALE
Adzakweza malipiro a anthu ogwira ntchito m’boma ndicholinga choti munthu azidzakwaniritsidwa ndi malipiro ake ndipo asadzakhale ndichilakololako chosokoneza chuma chaboma.
Adzakhazikitsa malamulo okhwima opereka chilango kwa anthu omwe asokoneza chuma chadziko lino kuti ena adzatengere phunziro.

KUTUKULA CHUMA
Adzakhazikitsa ndondomeko yoyenera yobwezeretsa chuma chadziko lino mchimake komanso adzaika njira zotetezera chuma chadziko lino kuti chisamadzaonongeke mukatangale komanso njira zomwe anthu amagwiritsa posakaza chuma chadziko lino.


Adzalemba ntchito aphunzitsi ambiri ngati njira yochepetsa kuperewera kwa aphunzitsi nsukulu zadziko lino.
Adzabwenzeretsa ndondomeko yoti maphunziro adzakhale aulere kuyambira ku primary kukafika ku sukulu za ukachenjede kuti aliyense adzakwanitse kuphunzira.

ZAUMOYO
Aliyense ogwira ntchito m’boma ndi makampane omwe si aboma adzathandiza 1% kuti boma lidzakwanitse kugula mankhwala kuti nzipatala zaboma mudzakhale mankhwala aulere okwanira omwe amaperekedwa kunzika muzipatala zonse zaboma zadziko lino.
Madotolo, anamwino komanso ogwira ntchito m’boma adzakwezeredwa malipiro kuti asadzathawire maiko akunja.
Adzalemba ntchito madotolo komanso anamwino omwe amaliza maphunziro awo.

KUKONZA MALAMULO
Adzakhazikitsa njira yokuti chilungamo chizifikira aliyense posatengera mapezedwe ake achuma.

KUTUKULA ULIMI
Adzakhazikitsa ulimi wamakono okuti dziko lino lidzakhala ndi zokolola zambiri zomwe zidzakwanira kudyetsa dziko lino komanso kugulitsa kunja zomwe zidzathandize dziko lino kupeza ndalama yakunja.

KULEMBA ANTHU NTCHITO
Boma lake lidzalemba ntchito anthu posayang’ana komwe munthu wachokera koma maphunziro ndikuthekera kwake. Adzafewetsa malamulo amakampani ndicholinga choti makampaniwo adzatukuke kuti pamapeto pake makampaniwo adzakwanitse kulemba ntchito anthu ambiri.

Adzalimbikitsa ntchito zamanja kuti achinyamata ambiri adzakhale odziimira paokha.

KUKONZA UBALE WAMAIKO AKUNJA
Adzapanga maubale ndimaiko okhawo omwe akhoza kupindulira dziko lamalawi.
Adzakonza ubale ndimaiko akunja pochepetsa ziphinjo zomwe amalawi amakumana nazo popanga mabusiness kunja komanso kuti maiko omwe tiri paubale katundu wake asadzakhale ndimsonkho zomwe zidzapangitse katundu adzatsike mitengo.

Ena kumafusa izi zidzatheka bwanji?
Izi zidzatheka chifukwa njira zili mmwambazi zidzaonjezeretsa ndalama yakunja komanso sipadzakhala ndalama yoonongeka kudzera mu katangale.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Please disable your adblocker or whitelist this site!