Wolemba: Leo Mkhuwala
Phungu woimila dela la Chikwawa Nkombedzi ku nyumba ya malamulo, Mayi Abida Mia watsindika kufunika kwa anakubala pamene anakayendera amayi omwe abereka kumene komanso ena omwe akudikilira kubereka pa chipatala cha Ngabu m’boma la Chikwawa chomwe chiri m’dela lake.
Mia yemwenso ndi nduna yowona za madzi ndi ukhondo, anafika pa chipatalacho ndi mphatso zosiyanasiyana monga zitenje, shuga ndi zakumwa zomwe adapereka kwa amayi osachepera makumi awiri, anati kwa mwana aliyense, nakubala ndi wofunika kwambiri chifukwa chobereka mwana ndi kumulera, popilira zowawa zambiri kufikira atakula.
“Palibe mphatso ina ya mtengo wapatali kuposa mphatso ya moyo yomwe nakubala amaipereka kwa mwana wake,” anatero Mayi Mia ndi kupitilira: “N’chifukwa chake mwana aliyense pa tsiku la anakubala akuyenera kukumbukira mayi wake chifukwa cha mphatso ya moyo komanso ntchito yaikulu yolera mwana yomwe mayi amagwira.”
M’chipinda cha matenite pa chipatala cha Ngabu, nkhope za amayi zinali zowala ndi chimwemwe pamene phungu wawo anafikira mayi aliyense mwapadera ndi kucheza naye komanso kunyamula khanda m’manja mwake ngati njira imodzi yogawana nawo chimwemwe pa tsiku la anakubala.
Pa 15 Okotobala chaka ndi chaka, dziko la Malawi pamodzi ndi dziko lonse limakumbukira mwapadera kufunika kwa mayi ngati nakubala.