Akuluakulu m’boma akukanirana komanso kukankhirana zokhudza lipoti la ndalama zomwe zidagwira ntchito ku mkumano wa United Nations General Assembly m’dziko la America komwe President Lazarus Chakwera ndi anthu ena 37 adapita.
Pafupifupi mwezi watha tsopano President Chakwera atabwera ku ulendowu koma nduna zake zikuchita jenkha kupereka lipoti za momwe misonkho ya aMalawi idagwilira ntchito.
Poyambilira, nduna zinayi motsogozedwa ndi m’neneri wa boma, Gospel Kazako zidalephera kuyankha mafunso a olemba nkhani ndipo zidati nduna yaza chuma, Sosten Gwengwe ndi yomwe ipereke lipoti-li.
Koma masiku angapo apitawa, akuluakulu ku unduna waza chuma adati iwo ntchito yawo nkupereka ndalama ku maunduna basi osati malipoti pa momwe ndalama-zi zagwilira ntchito.
Izi zikuchitika pomwe malipoti akuti ma allowance a anthu omwe adapita ku ulendowu adawakweza ndi 50 percent.
Koma mkulu wa bungwe la Centre for Social Accountability and Transparency-CSAT, Willy Kambwandira adati nzomvetsa chisoni kuti adindo akubisa zinthu zomwe ndizokhudza aMalawi zomwe anati zikusemphana ndi mfundo za boma zochita zinthu poyera.
Boma lidalepheranso kupereka lipoti lokhudza ndalama zomwe zidagwira ntchito pa mwambo wa chaka chino okondwera kuti dziko lino latha zaka 58 lili pa ufulu odzilamulira lokha.