Boma laitanitsa ogwira ntchito ku ADMARC okwana 1000 kuti athandizire kugawa zipangizo za ulimi zotsika mtengo mu ndondomeko ya AIP.
Nduna yaza ulimi, Sam Kawale yatsimikiza izi dzulo ku nyumba ya malamulo.
M’mbuyomu, nduna yakale yaza ulimi, Lobin Lowe idayamba yaimitsa anthu onse ogwira ntchito ku ADMARC ati pofunanso kukonza ntchito za bungweli.
Kodi chiganizo choitanitsa anthuwa boma lisadamalize kukonzanso ADMARC nkolondola?