Malawi Freedom Network
Giving you daily news that rock the world

MCP Yati Dpp Inkapwanya Dala Malamulo

Chipani cha MCP chati chikudziwa bwino kuti kuwonjezera madera a phungu komanso makhansala kufuna ndalama zochuluka komabe nkofunika mogwirizana ndi malamulo kuti ganizo la bungwe la MEC ligwire ntchito basi.

M’neneri wa chipanichi, Maurice Munthali wadzudzulanso chipani cha DPP ati posafuna kulemekeza malamulo m’mbuyomu ponena kuti zimapangitsa kuti anthu asamalandire zitukuko mofanana.

Posachedwapa, nyumba ya malamulo idavomereza lipoti la MEC lowonjezera madera a aphungu kuchoka pa 193 kufika pa 229 ndipo madera a makhansala afika pa 509 kuchoka pa 462.

Koma DPP yati kuwonjezera maderawa nkusaganiza kamba koti pakadalipano dziko lino likudutsa kale m’mavuto adzaoneni pachuma.

Leave a Comment

* By using this form you agree with the storage and handling of your data by this website.

This website uses cookies to improve your experience. We'll assume you're ok with this, but you can opt-out if you wish. Accept Read More