Nduna yowona za chitetezo cha mdziko, Ken Zikhale Ng’oma yalandira mendulo ya ulemu kamba ka ntchito yomwe akugwira pogwira ndi kutumiza ku Rwanda anthu omwe akuganiziridwa kuti anapalamula milandu yokhuza nkhondo.
Malinga ndi Ng’oma, anthuwa akhala akufunidwa kuyambira mchaka cha 1994 ndipo boma likusaka anthu ena asanu kuti nawo atumizidwe ku Rwanda.
Malinga ndi Ng’oma, mphotoyi apereka ndi akulu akulu a dziko la Rwanda.
Dziko la Rwanda linalengeza kuti yemwe azapeze anthuwa azalandira chionamaso cha ndalama zokwana 2.5 million zamdziko la Amerika zomwe ndi pafupi fupi 2.5 billion kwacha.
Lachitatu lino anthu ena okwana makumi anayi akuyembekezeka kutumizidwanso ku Rwanda.