Ophunzira okwana 1,145,220 ndi amene anatenga nawo gawo mu masewero osiyana-siyana monga a mpira wa miyendo, manja ndi ena ambiri mu mpikisano wa chaka chino wa masukulu, Youth Games.
Ophunzirawa ndi ochokera masukulu okwana 9,820 ndipo mwa chiwerengerochi 2,800 ndi a ku pulaimale, pamene 7,020 a sekondale.
Team ya North East Education Division (NEED) ndi Central West Education Division (CWED) apambana zikho ziwiri aliyense, koma NEED yavala ufumu kamba koti inatolera mapointi ochuluka kuposa CWED.
CWED inachita bwino kumasewero a chess komanso mpira wa manja ku sululu za pulaimale, pamene NEED inaphula ku masewero a volleyball komanso othamanga.
Shire Highlands Education Division Primary School ndiyomwe yachita bwino kumasewero a mpira wamiyendo, pamene CEED zawo zawayendera ku basketball.
Ndipo SEED yateteza ukatswiri kumasewero ampira wamiyendo ku sukulu zasekondale, pomwe SWED yavala ufumu kumasewero a mpira wa manja.
Unduna wa zamasewero wati uli ndi chikhulupiliro kuti ndalama zokwana K223 million zomwe boma likulowetsa kumasewerowa zithandizira kusula osewero oti azitha kubweretsa mamendulo ochuluka akapita kukatenga nawo gawo kumpikisano ya kunja kwa dziko lino.
M’modzi mwa akulu-akulu kuchokera ku unduna wa zamaphunziro, Joseph Mazaza, walankhula izi dzulo, lachiwiri, pa bwalo la Mzuzu pamene pamachitikira ndime yotsiriza ya mpikisanowu.
Mazaza wati ana omwe achita bwino kuchokera sukulu zosiyana-siyana apita m’mibindikiro (camp) ndicholinga choti akawasule luso lawo kuti azichita bwino pa mimpikisano yosiyana-siyana.
Mkulu wa Malawi Schools Sports Association (MASSA), Braxon Malamula, wayamikira boma kamba ka ntchito yotamandika yomwe akugwira popereka thandizo la ndalama ndicholinga chofuna kutukula luso la ana ochita masewero osiyana-siyana.
Ofalitsa nkhani ku Malawi National Council of Sports (MNCS), Edgar Ntulumbwa, wati pakufunika kugwirana manja ndi makampani ndicholinga choti ayambe kuthandiza masewero osiyana-siyana m’dziko muno.