FB IMG 1724503663954

Nyumba Ya Malamulo Ija Yasanduka Yoswera malamulo

Aphungu ena a nyumba ya malamulo abwera poyera mkuulura kuti amapatsidwa kanganyase kuti athandizire kudutsitsa malamulo ena ku nyumba ya malamulo.

Ena mwa aphunguwa atsina khutu nyumba yosindikiza nkhani ya Nation kuti amapatsidwa chiponda-m’thengo kuchokera ku magulu osiyanasiyana kuphatikizapo boma kuti avomele mosavuta ena mwa malamulo okomera boma.

Aphunguwa, omwe sanatchulidwe maina, ati mwachitsanzo, nthawi inayake boma lidawaitana kuti akachite phwando pa Hotel ina powathokoza kuti avomeleza ndondomeko yaza chuma ya chaka cha 2024/2025.

Pa phwandoli, phungu aliyense akutinso adafumbatitsidwa k400,000 aliyense kuti agulire madzi akumwa.

Kafukufukuyu waonetsanso kuti mzaka za 2016, boma lamu nthawiyo lidatengera aphungu malo osiyanasiyana kuwaonetsa zitukuko koma kwinaku akutikitira ndalama zochuluka za allowance.

Akuti nthawi inanso, aphungu omwe amakonda kuyambitsa chiwoye m’nyumba ya malamulo maka pa nthawi yomwe mtsogoleri wa dziko akuyankhula amafumbatitsidwa kangachepe chomwe chimakhala ngati chitseka pakamwa.

M’mbuyomu, anthu ena omwe adakhalako aphungu a nyumba ya malamulo akhala akuthira mchenga mu m’memo wa gulu pomwe amaulura kuti amalawi asamadabwe ndi khalidwe la aphungu ena longovomeleza zilizonse, ponena kuti amakhala apatsidwa kanganyase.

More From Author

FB IMG 1724501811734 300x169

Driver gets one year jail term for reckless driving

Manchester City V Arsenal The Fa Community Shield 6 300x200

Mikel Arteta hints at a fresh position change for Timber

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Ella Brown

Project Manager

Darkness cannot drive out darkness; only light can do that. Hate cannot drive out hate: only love can do that.