
Njanjeyo siyawo ndiya Mozambique _ Namalomba
Mneneri wachipani cha Democratic Progressive (DPP) Shadreck Namalomba wati ndiwodabwa kuti mtsogoleri wadziko lino akuwuza mtundu wa a Malawi kuti boma lake labweretsa mafuta agalimoto lachitatu kudzera panjanji.
Izi zikudza pomwe mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera lachitatu analandila sitima yapanjanji yobweletsa mafuta agalimoto m’boma la Nsanje yomwe akuti patha zaka zoposa 40 isanakuyenda.
Komatu malingana ndi a Namalomba izi sizoona ponena kuti njanjeyi yamanga ndi boma la Mozambique kuchoka ku Beira kufika pa malire adziko lino ndi dziko la Mozambique.
“Komasotu a Kongelesi akulephela kuwauza aMalawi chilungamo kuti zanjanjezi tidayambitsa ndife a DPP ndipo tidzazimalizitsaso tokha tikadzalowa m’boma 2025” atelo a Namalomba.
Mwazina a Namalomba ati zikanakhala bwino boma lidakamanena chilungamo chifukwa amalawi akudutsa kale mu nyengo zowawa.
Read also: UTM seeks clarification from Michael Usi over ‘boma ndi lomweli’ remarks
Read also: Exploring the World’s Largest Banana Tree in Papua New Guinea
Read also: UNDP Hands Over 220 Kilowatt Bondo Min-Grid to Malawi government.








