Masewero alero atulutsa zigoli khumi ndi ziwiri
Zigoli khumi ndi ziwiri ndizomwe zagoletsedwa masewero omwe analipo lachitatu pa 25 September 2024 mu TNM Super league. FCB Nyasa Big Bullets yagonjetsa Creck Sporting Club 3-2 pamasewero omwe anachitikira pa bwalo la Kamuzu mu nzinda wa Blantyre. Maxwell Gasten Phodo, Babatunde Adepoju komanso Ernest Petro anagolestera mapale, pamene Muhammad Sulumba anagoletsa zigoli ziwiri yekha […]