Zigoli khumi ndi ziwiri ndizomwe zagoletsedwa masewero omwe analipo lachitatu pa 25 September 2024 mu TNM Super league.
FCB Nyasa Big Bullets yagonjetsa Creck Sporting Club 3-2 pamasewero omwe anachitikira pa bwalo la Kamuzu mu nzinda wa Blantyre.
Maxwell Gasten Phodo, Babatunde Adepoju komanso Ernest Petro anagolestera mapale, pamene Muhammad Sulumba anagoletsa zigoli ziwiri yekha kuti masewero athere 3-2.
Masewero ena omwe analipo pa bwalo la Balaka, Kondwani Chilembwe, Richard Lapson komanso Clever Chikwata anagoletsera Bangwe All Stars kuti igonjetse igonjetse Baka City 3-0.
Peter Katsonga anali katswiri ofunikira pamene anagoletsa zigoli ziwiri yekha kuti timu yake ya Mafco FC igonjetse Mighty Tigers 2 kwachilowere pamasewero omwe anachitikira pa bwalo la Chitowe m’boma la Nkhotakota.
Ndipo pa bwalo la Civo, Christopher Mtambo komanso Gregory Nachipo anagoletsera Kamuzu Barracks kuti igonjetse Premier Bet Dedza Dynamos.
Silver Strikers ndiyomwe ikutsogola pa m’ndandanda wa ma timu ochita bwino mu TNM Super league ndi mapointi 48 pamasewero 20 omwe asewera, pomwe Mighty Mukuru Wanderers ili panambala yachiwiri ndi mapointi 41.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!