Zavuta kumpanda

Timu ya Kamuzu Barracks (KB) yatsanzika mu chikho cha Castel Challenge pamene dzulo Civil Service United yakana zowalirana poyedzeka KB 2-1.

Damiano Kunje yemwe omunyadira amati amwala ndiyemwe walasa mthiti za Kamuzu Barracks pomwe kawiri konse anagwedeza ukonde.

Mphunzitsi wamkulu wa KB, Charles Kamanga, wati anali masewero oti akanatha kupambana koma sizinayende momwe anakonzera.

”Ngati ineyo mphunzitsi ndivomereze kuti mpira chaka chino kumapeto kuno wativuta ndithu,” watero Kamanga.

Kumbali yake Mphunzitsi wamkulu wa Civil Service United, Abas Makawa, wati timu yake sinapeze mipata yambiri yochinya koma wayamikira anyamata kamba kogwiritsa ntchito mipata iwiri yomwe apambana nayo.

”Timu yanga inalanda pakati chifukwa timatha kusokoneza mpira ulionse obwera pakati,” watero Makawa.

Apa ndekuti zadziwika kuti mu ndime ya ma Kota finolo timu ya Civil Service United ikhale ikukumana ndi timu ya Leyman Panthers yomwe yokhodzola matimu a MAFCO, Silver Strikers komanso Chitipa United.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *