By Burnett Munthali
Timu ya mpira wa miyendo ya amai ya Arsenal yafika mu ndime ya Semifinals mu mpikisano wa Uefa Champions League itagonjetsa timu ya Real Madrid ndi zigoli zitatu kwa duuu.
Izi zikutsatira kupambana kwa timu ya Real Madrid sabata yatha pamene inakwapula timu ya Arsenal ndi zigoli ziwiri kwa duuu.
Zateremu, Arsenal yapitilira ku ndime ina yachipulura popambana ndi zigoli zitatu kwa ziwiri powonkhesera (Aggregate) ndipo ikhala ikukumana ndi timu ya Lyon m’ma semifinals.
Mpikisano wa Uefa Champions League kwa gulu la amai ukusonyeza kupikisana koopsa komanso kupanda kudalirika kwa zotsatira, popeza magulu akuluakulu akupikisana mwaukali.
Kugonjetsa kwa Arsenal Real Madrid kukutanthauza kuti timu iyi ili ndi mphamvu yoti ipitirire kuchita bwino mu mpikisano wa chaka chino.
Ngakhale Real Madrid idawoneka ngati yomwe ikuchita bwino atakwapula Arsenal sabata yatha, zotsatira za pa masewero omaliza zikuwonetsa kuti mpira ndi wosadziwika.
Pamene Arsenal yakwanitsa kugonjetsa Real Madrid, ntchito yayikapo kuti idzakumane ndi timu yamphamvu ya Lyon, yomwe imadziwika kuti imachita bwino mu mpikisano wa Uefa Champions League.
Lyon ndi timu yomwe yakhala ikulamulira mpira wa amai ku Europe kwa zaka zambiri, kotero Arsenal iyenera kukonzekera bwino ngati ikufuna kupita ku Final.
Anthu okonda timu ya Arsenal akuyankhula molimbitsana mitima koma monong’ona pogwiritsa ntchito mwambi uja okuti “Aonenji wagwira mvuwu mu mono”, popenekera kuti mwina zotelezi zithanso kuchitika masabata akudzawa.
Zimenezi zikutanthauza kuti pamene timu ya amai ya Arsenal yagonjetsa Real Madrid, timu ya abambo nayo ikhoza kudutsanso njira yomweyo mu mpikisano wa Uefa Champions League.
Ngakhale mpira wa amai sikuti umapeza chidwi chofanana ndi wa abambo, kupambana kwa Arsenal kukusonyeza kuti mpikisano wa amai ukuyamba kutenga mphamvu komanso kutchuka.
Pamene chiyembekezo cha osewera ndi mafani cha Arsenal chikukwera, timu iyenera kukonzekera mwamphamvu kuti ipambane Lyon ndiponso kufika ku Final ya Uefa Champions League.
Ngakhale mpikisano wa Semifinals ukhoza kukhala wovuta, mafani a Arsenal ali ndi chiyembekezo kuti timu yawo ikhoza kubweretsa mbiri yakale popambana mpikisano wa chaka chino.