Prophet Shepherd Bushiri atsutsa njira zowunikira chilungamo ku South Africa

Olemba: Burnett Munthali

Prophet Shepherd Bushiri wadzudzula ntchito za chilungamo ndi za mabwalo a milandu m’dziko la South Africa kutsatira kusapezeka ndi mlandu pa milandu 32 yomwe mabwalo adzikolo amazenga mlaliki wina yemwe kwawo ndi ku Nigeria, koma amakhala m’dziko la South Africa, a Timothy Omotoso. Milandu imeneyi inaphatikizapo yogwilira, kuzembetsa anthu, ndi kuchita zachinyengo.

A Bushiri, omwe akutsutsana ndi chigamulo choti akazengedwe milandu m’dziko la South Africa, ati kumangidwa kwa a Omotoso kwa zaka zisanu ndi zitatu osapatsidwa belo kuli ndi umboni woti atsogoleri a zipembedzo ochokera kumayiko ena amachitiridwa nkhanza m’dziko la South Africa.

Iwo ayerekeza zomwe akumana nazo a Omotoso ndi zomwe akukumana nazo iwo, ponena kuti mabwalo a milandu a South Africa amachita ndale pochita zinthu zokhudzana ndi atsogoleri a zipembedzo omwe si a dziko lawo.

Mneneri Bushiri, yemwe anathawa m’dziko la South Africa mchaka cha 2020, wati iye akhoza kukakumananso ndi izi ngati angabwerere kumeneko kuti akazengedwe milandu. Iye akutsimikiza kuti milandu yomwe akuti akamuzengeyo inabwera nthawi yomwe anachoka m’dzikolo kubwera ku Malawi.

Iye wati mabwalo akuluakulu ku Malawi anagamula kuti alibe mlandu pa milandu khumi yomwe ankazengedwa, koma akudandaula kuti anthu a m’dziko muno, kuphatikizapo atolankhani, sakufuna kumakamba za izo.

“Amafuna anditsekere, andiyiwalitse, kunyazitsa dzina langa kufikira nditatsala opanda kanthu mpaka kundipha,” watero Bushiri, ponena kuti dziko la South Africa likufuna kumuona atagwa.

A Bushiri awonjezera kuti dziko la South Africa limafuna kuthana ndi anthu obwera m’dzikolo powamanga pa milandu yosadziwika bwino, makamaka pa nkhani zokhudza chuma.

Iwo ati, “Kukhala obwera m’dziko la South Africa ndi kukwanitsa kuchita bwino ndizofanana ndi kuzilemba kumbuyo kuti uzisakidwa ndi akuluakulu a dzikolo.”

Iwo wachenjeza motero, ponena kuti zimenezi zikutsimikizira kuti ndondomeko za chilungamo m’dziko la South Africa sizigwira ntchito mwachilungamo kwa alendo.

A Bushiri atsiriza ndi kuchenjeza a Omotoso kuti achoke m’dzikolo mwamsanga ngati apeza mwayi.

Mlandu wa Omotoso wawutsa mtsutso pa kagwiridwe ka ntchito za mabwalo a milandu ndi okhudzidwa ndi chilungamo m’dziko la South Africa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *