Chipani cha Malawi Congress Party chatilephera ndipo chinabwera kuzangoononga chuma cha dziko

By Comrade Jumbe

Abale ndi Alongo,

Tawona ndi maso athu, ndipo tamva ndi makutu athu. Chipani cha Malawi Congress Party chatilephera ndipo chalephera dziko lathu.

Zonse zomwe amalonjeza asanalowe m’boma zinali zogwira mtima ngati maloto okoma, koma tawonani lero zonse zija zasanduka kukhala maloto owopysa ndi malawi enieni amoto monga mwadzina lake la dziko lino.

Tinayembekezera chitukuko, koma ndi chitukuko chanji chokagula nacho feteleza mu butchery, ndi chitukuko chanji choti amalawi ndikumagona mma filling station kusowa mafuta, ndi chitukuko chanji chogwetsa kwacha ndi 50 palasenti kukhawulitsa ife amphawi.

Kodi ndege ya bwana vice president wathu mukuti chinachitika ndi chani kwenikweni,Nanga zakudya katatu ziri pati?

Tikanena za Neef ndi imeneyi yikutisawukitsa mmakwalalamu yasanduka bungwe lopangisa katapila nanga ndkuthandiza kwa mtundu wanji kupeleka 1 million kubweza 2 million, ife osauka tikungosawukilabe tinakulakwilani chiyani a congress.

Kunena zoona Pansi pa utsogoleri wa chakwera ndi MCP, a Malawi tikuvutika kuposa kale lonse. Mitengo ya chakudya, mafuta, ndi zinthu zofunika kwambiri yakwera.

Achinyamata alibe ntchito mungowazatsitsa ma stadium ntchito mutalembana kale pa chibale mulungu akulangani pansi pompano.

Amayi alibe chiyembekezo, ndipo tsogolo likuwoneka ngati mdima wa ndiwe yani.

Amati mbiri safuta ena akuti maloto sang’amba choncho amalawi Tisaiwale mbiri yoyipa ya MCP.

Chipani cha mcp kuyambila kale ndi chipani chankhanza Azigogo athu anazunzidwa, ena anataya miyoyo pansi pa atsogoleri wa chipini chimenechi, Lero anabwera atavala nsaru yatsopano yoyela ngati angelo koma ali ana asatana, akulu anati fisi ndi fisi ngakhale atasintha mtchire.

“Njoka ikasintha khungu, sichotsapo poizoni.”

Choncho amalawi pa 16 September, tiyeni tichite Kuyambitsanso Kachiwiri tisinthe dziko lathu. Tsiku limenelo lizakhale la kubadwa kwa tsopano kwa dziko lathu.

Tiyeni tichotse MCP ku utsogoleri komanso ku mndandanda wa zipani za ndale mmalawi muno, ndithu ngati simungamvere ndikunenazi sungani mawu anga amenewa mma dairy mwanu ndipo muzandikumbuka.

Tiyeni titeteze ana athu ku zowawa zomwe ife tikukumana nazo ndipo tiwateteze kuzowawa zomwe makolo athu anakumana nazo mu mbiri ya dziko lino.

16 September likhale tsiku lochotsa chinyengo, lolemba mbiri yatsopano ife ngati amalawi lizakhale tsiku lochotsa chakwera ndi chimwendo.

Tiyeni tilembe mbiri yatsopano ya ufulu, mtendere, ndi chitukuko chenicheni.

Nthawi yakwana yoti dziko lathu litha kuchira nafe eni ake ngati amalawi titha kuchila kumikwingwilima yomwe tikukumana nayo mmoyo wathu wa tsiku ndi tsiku ngati tonse pamodzi titapanga chiganizo choyenera pa 16 September pano.

My pen 🖊 is mightier than a sword.