By Suleman Chitera
Mneneri Shepherd Bushiri, mtsogoleri wa mpingo wa The Jesus Nation Church, walangiza andale kuti asiye kunamiza a Malawi ndi malonjezano abodza pomwe dziko likukonzekera chisankho mu mwezi wa mawa.
Kudzera pa tsamba lake la Facebook, Bushiri wanena kuti andale ayenera kuyankhula zoona ndikulonjeza zinthu zomwe angakwanitse kuchita akasankhidwa, osati kubwereza mabodza.
“Lekani kuuza anthu zinthu zomwe inu simungakwanitse kuchita mutasankhidwa. Dziko lathuli lili m’mavuto aakulu ndipo likufunika mtsogoleri amene angatsogolere mwachilungamo komanso mwachikondi. Lonjezani zomwe mungakwanitse.” – Shepherd Bushiri
Ichi ndi koyamba kuti Bushiri, yemwenso ndi wochita malonda komanso ntchito zachifundo, ayankhule poyera zokhudza zisankho zomwe zikuchitika pa 16 September.