750 Million Kwacha Siidabwezedwe Ku Dziko Lino

1 min read

Wapampando wa komiti ya za ulimi ku nyumba ya malamulo a Sameer Suleman wati ndi zomvetsa chisoni kuti a ndale ena amalowetsa ndale pa nkhani zofunikira zokhudza a Malawi.

Iwo amayankhula izi pomwe zotsatira za kafukufuku yemwe boma linakhazikitsa kuti lipeze kuti nkhani yokhudza ndalama yokwana 750 million kwacha yomwe idaperekedwa ku butchala ina yakunja kuti ibweretse fetereza m’dziko muno ili pati.

Iwo ati sipakuoneka chidwi chofuna kulondoloza za ndalamayi zomwe zikupereka chithunzi thunzi kuti nkutheka a ndale ena adapindulapo.

Nduna ya kale ya za ulimi a Robin Lowe adavomereza kuti undunawu udapereka ndalamazi ku kampani yakunjayi kuti ibweretse fetereza yemwe adali wa mu ndondomeko ya AIP koma zidadziwika kuti kampaniyo
Kulibeko.

Pakadali pano a Malawi ambiri adataya mtima kuti ndalama-yi idzabwezedwa.

You May Also Like

More From Author

+ There are no comments

Add yours