Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, ku m’mawaku akuyembekezeka kutsogolera mwambo otsegulira ndondomeko ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya AIP m’boma la Dedza.
Chaka chino, ndondomeko-yi yakhudzika ndi mavuto angapo kuphatikizapo malipoti akubedwa kwa ndalama zokwana K30 billion ngakhale boma lidakana izi ponena kuti ndalama zomwe likudziwa ndi K750 million.
Padakali pano, thumba la feteleza m’dziko muno lafika pa K75,000 ndipo alimi omwe apindule ndi AIP akhale akugula thumba pa K15,000.
Koma nduna ya za ulimi, Sam Kawale, yatsimikizira aMalawi kuti feteleza yemwe boma lagula komanso yemwe ena apereka ngati thandizo ndi okwanira kuti pasakhale zosamwitsa zili zonse.
Boma lidaika K109.4 billion ku AIP chaka chino yogulira feteleza oti apindulire alimi 2.5 million.
Chiwerengerochi chidatsika kuchoka pa 3 million kaamba ka kugwa kwa ndalama ya Kwacha komanso kukwera mtengo kwa feteleza.