Boma alipempha kuti liyambe kuika msonkho pa malonda ang’ono-ang’ono monga a chips cha pachiwaya, mizimbe komanso chimanga.
Henry Kamkwamba mphunzitsi wa zaulimi komanso zachuma ku sukulu ya ukachenjede ya LUANAR, wanena izi pomwe sukuluyi imapereka maganizo ake kuti pachitike chani kuti ndondomeko ya chuma ya chaka cha 2023/2024 iyende bwino.
Kamkwamba wati, malonda ang’ono-ang’ono-wa akupanga ndalama zochuluka koma sakupereka msonkho ku boma.
“Mukati muone ochita malonda ang’ono-ang’ono-wa amapita kuchipatara kukalandira thandizo, ana awo amapita ku sukulu za boma koma sakulipira nawo msonkho, ndiye opeleka msonkho ndi ochepa koma ofuna ma services aboma ndi ambiri. Ndondomeko yachuma ikudzayi iunikirepo pamenepo. Pakufunika kuti ochita business zing’onozing’ono azilembetsa malonda awo ku boma kuti boma liziwadziwa,” watero Kamkwamba.
Kamkwamba watinso nkofunika kuti boma likhazikitse komiti yapadera yomwe itsogoleredwe ndi Mtsogoleri wa dziko lino (Presidential Taskforce on Agriculture) kuti idziyang’anira ntchito za ulimi Komanso kafukufuku wa zaulimi.
Malingana ndi Kamkwamba nzomvetsa chisoni kuti mpaka pano dziko la Malawi silidapezebe njira yothandirana ndi tizilombo toononga mbeu monga Ntchemberezandonda, pomwe dziko lili ndi akatswiri woti atha kuchita kafukufuku pa izi.
Poyankhapo, Sosten Gwengwe nduna ya zachuma wati nkofunika kuti bungwe lotolera msonkho la MRA lichite zokambirana ndi unduna owona za maboma ang’ono Komanso chitukuko cha mmidzi kuti pakhale ndondomeko yoyenera yotolera msonkho ku malonda ang’ono-ang’ono-wa.