Atatu ali mmanja mwa apolisi kamba kopha munthu

Anthu atatu anjatidwa kamba kowaganizila kuti apha a Charles Assan azaka 32 omwe amagwira ku Bank ya First Capita Bank m’boma la Dowa.

Mneneri wa Polisi ku Mponera a Macpatson Msadala ati atatuwa ndi a Jafali Mtungwe emwe ndi dalaivala wa Bungwe la NEEF , Nelson Jossam ndi chibwenzi chake Halima Kamwana.

Nkhaniyi ikuti Malemuwa ndi anthu ena awiri a Nelson Jossam ndi a Halima Kamwana atamaliza kumwa mowa pa Malo ena a Sunrise anakonza zomapita kwawo koma sanapeze Taxi iliyonse yoti iwatenge.

Ali mofufuzabe Taxi-yi iwo anaona Galimoto ina ya Toyota Hilux Pickup yomwe inali ya bungwe la NEEF ndipo imaendetsedwa ndi a Jafali Mtungwe ndipo atapepha anawaloledza kuwatenga kuti akawasiye ku dera la Nkhamanga.

Ali mu Galimotoli anasephana maganizo zomwe zinapangitsa kuti dalaivalayi awatulusemo ndipo atatulukamo woyendetsayi anayendetsa Galimoto yomwe inagunda Malemuwa.

Chipatala Chamadisi Mission chapedza kuti a Assan amwalira kamba kovuladzidwa pogundidwa komanso thupi lawo lapezeka ndimabala olumidwa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *