“Chakwera Ayimanso Pa Chisankho Cha 2025”

Komiti yaikulu ya chipani cha Malawi Congress -MCP, yabwereza kuti yagwirizana pa chiganizo choti mtsogoleri wa chipani-chi, Lazarus Chakwera, yemwenso ndi mtsogoleri wa dziko lino, aimire-nso chipani-chi pa chisankho chamu 2025.

Mlembi wamkulu wa MCP, Eisenhower Mkaka, wanena izi ku maofesi a chipani-chi ku Lilongwe, pambuyo pa mkumano wa komiti-yo yomwe Chakwera anatenga nawo mbali.

Iye wati komiti-yi inagwirizana pa chiganizo-chi m’mbuyomu, ndipo pa mkumano wa Lachitatu mamembala a komiti-yi aitsimikiza-nso.

Komabe, Mkaka wati mamembala a MCP ofuna mpando wa mtsogoleri wa chipani-chi ndi oloredwa kuti akapikisane ndi Chakwera ku msonkhano waukulu, omwe dongosolo lake alengeze mtsogolomu.

Malingana ndi malamulo a chipani cha MCP, munthu amayenera kukhala pa mpando wa mtsogoleri wa chipani-chi kwa zaka khumi, ndipo potengera izi pofija mu 2025 President Lazarus Chakwera akhala kuti wamaliza zaka khumi zokhala pa udindo-wu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *