Chipani chatsopano Cha N D P Achikhazikitsa Mdzikolino

Chipani chatsopano chomwe akuchitcha National Development Party (NDP) ndipo mtsogoleri wake ndia Frank Mwenefumbo achikhazikitsa mdzikolino.

Ofesi ya mkulu oona zakalembera wa zipani zandale yapeleka kale chilolezo ku chipanichi kuti chitha kuyamba kugwira ntchito zake mdzikolino kuyambira pa 1 March, 2024.

Mlembi wamkulu wachipanichi a Gerald Chilongo watsimikiza lero kuti chipanichi achikhazikitsa mwazina pofuna kugwira ntchito ndi a Malawi polimbana ndimavuto monga a zachuma komanso kusakazika kwa zachilengedwe.

Komabe a Chilongo ati pakadalipano chipanichi chaika chidwi polimbikitsa nthambi zake ndipo pakadalipano sichidapange chiganizo ngati chizapange mgwilizano ndi zipani zina kapena ayi.

Mtsogoleri wachipanichi a Mwenefumbo, anakhalapo mneneri wachipani cha UTM.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *