Dekhani, Ndikukumbukira Malonjezo Anga-Katsonga

Anthu m’dera la Zalewa m’boma la Neno ati akupitilira kusautsika ndi vuto lakusowa kwa madzi aukhondo pomwe phungu wa kunyumba ya malamulo kumwera kwa bomali, Mark Katsonga Phiri wati akukumbukira za malonjezo omwe adapereka koma wapempha anthuwa kuti adekhe.

AKatsonga, omwenso ndi nduna yaza malonda ndi mafakitale, anena izi pa mkumano omwe anachititsa ndi mafumu komanso anthu akudera la Zalewa pomwe amawafunila mafuno abwino a chikondwerelo cha khilisimisi ndi chaka cha tsopano.

Iwo anati akukumbukira bwino kuti adalonjeza kubweretsa madzi a m’mipope komanso sukulu ya secondale pa Zalewa koma wati mliri wa Covid-19 ndi omwe wakhala ukupinga zina mwa ntchito za chitukukozi.

Apa, iye wapempha anthu akuderali kuti adekhe ponena kuti malonjezowa akwaniritsidwa posachedwa.

Ndipo poyankhapo pa nkhani ya kuchedwa kwa zipangizo za ulimi zotsika mtengo zomwe anthu kuderali anadandaula kuti sanayambe kugula, phunguyu wati achita chothekera kuti feteleza afikile m’madera ambiri kuti anthu adzipeza zipangizozi mosavuta.

M’mawu ake, Group Village Headman Zalewa inayamikila phunguyu kaamba kobwera kudzacheza ndi anthu kuderali koma anati ayang’anila kuti malonjezowa akwaniritsidwe mwachangu ponena kuti anthu akuderali akusautsika pa nkhani ya madzi aukhondo ndi maphunziro a secondale kaamba koti derali lilibe sukulu ya secondale ndi imodzi yomwe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *