Kusowa Kwa Shuga Kuja Kunali Kochita Kukonza- Namiwa

Wolemba: Vincent Poya- Thyolo.

Mkulu wa bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative ( CDEDI) Sylvester Namiwa wati ndi zokhumudwitsa kuona mitengo ya shuga ikupitilira kukwera ngakhale kuti akupitilira kusowa.

Namiwa walankhula izi pothilirapo ndemanga pa kalata yomwe kampani yopanga shuga ya Illovo Sugar Malawi yatulutsa yokhudza kukwera kwa mitengoyi.

Mwa zina a Namiwa waloza chaka nduna yoona za malonda ndi mafakitale a Sosten Gwengwe maka posalabadira a Malawi pomwe alora kuti Illovo ikweze mitengoyi.

Mmawu awo a Namiwa omwe amamveka mokhumudwa atinso vuto lakusowa kwa shuga lomwe lakhudza dziko lino ndi lochita kukonza.

” Ndinene pano kuti shugayu akusowa dala ndi cholinga choti akapezeka ochepa anthu azigula ngakhale ali okwera polimbira poti bola wapezeka, ” watero Namiwa.

Namiwa wati ndi odabwa kuona kampani ya Illovo ikukweza mtengo wa shuga pomwenso dziko lino lakumana ndi vuto la kusowa kwa shugayu ponena kuti kukanakhala bwino shugayo akanamapezeka kenako ndikukweza mitengo.

Koma mmodzi mwa akatswiri pa nkhani ya zachuma mdziko muno Kingsley Jasi anati sizodabwitsa kuona mitengo ya shuga ikukwera poti izi zikutsatiranso kawuniwuni omwe banki yaikulu pa dziko lonse la pansi yemwe analosera za izi m’mbuyomu.

“Mitengo ya zinthu ipitiriza kukwera chifukwa cha zinthu monga kusowa kwa ndalama za kunja komanso paja ndalama yathu inatsika mphamvu nde izi ndi zinthu zosadabwitsa.” Anatero Jasi.

Poyankhapo pa nkhani yoti Illovo Sugar Malawi inachitira dala kusowetsa shuga pa msika, Jasi anati izo ndi zomwe anthu atha kumaganiza ndipo ngati zili ndi umboni ndiye kuti izinso ndi milandu .

A Lekani Katandula omwe amalankhulira kampani ya Illovo anati sizoona zomwe a Namiwa ayankhula poti ati ndi mlandu kutero ndipo ngati kampani sangachitire dala kuchita zimenezo.

Iwonso anati mitengoyi yakwera chotere potengera ndi kukweranso kwa zipangizo zogwiritsa ntchito popanga shugayi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *