Matimu Akonzeka Kuonetsa Luso Lapamwamba – Mwambetania

Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo osewerera mu mchenga lati zokonzekera zokhuza ndime yomaliza ya mpikisano wa dziko lonse zafika kumapeto.

Bungweli lalengeza kuti masewero a HTD Beach Soccer National Championship akhale akuchitika kumapeto a sabatayi ku Mkopola Leisure center mu boma la Mangochi.

Mlembi wa bungweli, Wakisa Mwambetenia wati kukhala ndi umwini kwa matimu ambiri kwathandizira kuti mpikisano komanso kayendetsedwe ka matimu kasinthe zomwe zikuthandizira kukweza chikoka komanso mpikisano pakati pa matimu.

“Inde zovuta sizilephera monga kuchedwa kubwera kwa ndalama zopita ku matimu koma padakali pano mpikisano nde ulipo kamba koti matimu ambiri apeza osewera apamwamba omwe akopeka ndikuchita bwino kwa osewera omwe anakachita nawo masewero a Cosafa mdziko la South Africa.” Anatero Mwambetania

Iye watinso masewerawa akuchitikira ku Mangochi kutsatira madzi omwe avuta ku Karonga komwe masewerowa amayenera kuchitikira pachiyambi.

Timu ya Beach Eagles ndi yomwe ikusunga ukatswiri wa chikho’chi.

Matimu omwe atenge nawo mbali mu mpikisano wa chaka chino ndi; Sunbird Mkopola(Mangochi), Tourism(Salima), Beach Eagles(Chintheche), Deep Bay ndi Noil(Karonga) ndi Vinthenga(Nkhotakota).

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *