Mitawa Ayima Opanda Opikisana Naye

Ogwilizira mpando wa mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi(Sulom), Colonel Gilbert Mitawa ayimira pa mpando wa mtsogoleri wa bungweri opanda opikitsana nawo.

Izi zikutsatira chikalata chomwe atulutsa a Crowe Howarth Malawi omwe amayendetsa ndondomeko yolandila ma kalata a anthu ofuna kuzayimila pa maudindo ku bungwe la Sulom omwe anatseka kulandila ma kalatawa.

A Mitawa omwe amagwilizira udindo’wu kutsatira kwa kuchoka kwa Fleetwood Haiya amene pano ndi mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi akuyembekezeka kupitiliza ngodya zomwe anasiya a Haiya zofuna kusintha mpira.

Pa udindo wa mamembala a komiti yayikulu ya bungweri pali anthu atatu omwe akupikisana omwe ali Isaac Mdindo, William Nhlane ndi Charles Manyungwa.

Zisankho zizachitika pa 30 March, 2024 mu mzinda wa Lilongwe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *